Zomba, Malaŵi

From Wikipedia

Zomba ndi mzinda omwe uli m'chigawo Chakumwera kwa dziko la Malawi.

Mzinda wa Zomba udakhazikitsidwa m'chaka cha 1890 pomwe Angerezi anayamba kulamulira dziko la Malawi (kale ankati Nyasaland). Zomba anali likulu la ulamuliro wa chitsamunda cha Angerezi ku Malawi mpaka pameneko, mtsogoleri woyamba wa fuko la Malawi a Dokotala Hastings Kamuzu Banda, anasamutsa likulu la Malawi kupita ku Lilongwe. Likulu la asilikali a Malawi lili ku Zomba. Nyumba yamalamulo inali ku Zomba nthawi yaitali mpaka pamene mtsogoleri wachiwiri wa dziko la Malawi Bakili Muluzi anaisamutsira ku Lilongwe.