Malawi Congress Party
Malawi Congress Party (MCP) ndi chipani cha ndale cha ku Malaŵi. Dzina lake la kale la chipanichi linani Nyasaland African Congress, koma chinasintha kukhala MCP pa nthawi yomwe a Hastings Kamuzu Banda anali mundende ku Gwelo my Southern Rhodesia. Anakhazokitsa chipanichi ndi a Orton Edgar Chong'oli Chirwa and a Aleke Banda.
Chipanichi chinapambana pa chisankho mu chaka cha 1961 ndipo chinatenga mipando yonse pa chisankhochi. Kupambana kumeneku kunapangitsa kuti dziko la Malaŵi lipatsidwe ufulu wodzilamulira lokha kuchokera ku boma la chitsamunda. Mu 1966, chipanichi chinapatsidwa mphamvu yokhala chipani chikhacho mu dziko la Malaŵi. Anthu wonse akulu akulu amayenera kukhala mbali ya chipanichi ndipo amayenera kunyamula ziphaso zosonyeza kuti iwo analidi otsatira chipanichi.
Chipani cha MCP chinatha mphamvu 1993 pamene kunachitika chisankho chomwe anthu ambiri anasankha kuti boma la Malaŵi likhale la zipani zambiri. Mu 1994, chipanichi chinagonjetsedwa m ndi chipani cha zipani zambiri chomwe chinachitika mu dziko la Malaŵi.
Ngakhale zinakhala chonchi, chipani cha MCP chinakalibe ndi mphamvu mu dziko la Malaŵi ndipo chili ndi mphamvu zambiri mu chigawo cha pakati cha dzikoli kumene kuli aChewa ndi aNyanja ambiri.
Pa chisankho chomwe chinachitika mu 2004, mtsogoleri wa chipanichi a John Tembo (amene anali wogwirizana kwambiri ndi a Banda) anapeza 27.1% ya mavoti onse ndipo chipanichi chinapeza mipando 60 kwa mipando 194 yomwe ya a phungu wa nyumba ya malamulo.