Wikipedia:Kalembedwe ka nkhani

From Wikipedia
NOTE TO READERS:THIS IS A PAGE EXPLAINING HOW TO WRITE ARTICLES TO HELP NEW USERS!

Malo ano akufotokoza za mmene mungalembele nkhani pa Wikipediya, makamaka amene angoyamba kumene


  • Lembani masamba abwino. Masamba abwino kwambiri a encyclopedia ali ndi zothandiza, zolembedwa bwino.
  • Osagwilitsa ntchito makina ngati google translator! Nkhani yolembedwa pogwilitsa ntchito translator wina aliyense siikhala yomveka bwino (Don't use machine translations!). Nkhani zotelo zizafufutidwa pano mopanda kudziwitsa olembayo komanso kupitiliza kutelo n'kuphwanya malamulo a Wikipediya.
  • Gwiritsani ntchito masambawa kuti muphunzire ndi kuphunzitsa. Masambawa angathandize anthu kuphunzira Chichewa. Mutha kuigwiritsanso ntchito pangani Wikipedia yatsopano kuthandiza anthu ena.
  • Khalani wolimba! Nkhani yanu siyenela kukhala yangwiro, chifukwa olemba ena adzakonza ndikupanga bwino. Ndipo chofunika kwambiri, musaope kuyamba ndi kupanga nkhani bwino.