Jump to content

Lilongwe

From Wikipedia
(Redirected from Lilongwe (Malaŵi))
Lilongwe
Lilongwe

Lilongwe ndi boma lina la dziko la Malaŵi.

Lilongwe, ndi mzinda omwe umapezeka m'dziko la Malaŵi ndipo uli ndi anthu Pafupi fupi 1,600,000 ndipo ndi kapitolo ya dziko la Malaŵi. Mzinda wa Lilongwe umapezeka m'dera la pakati m'dziko la Malaŵi,ndipo udakhala pa Mstinge wawukulu wa Lilongwe, pafupi ndi malile a Malaŵi ndi Mozambique ndi Zambia. Mseu wawukulu wa M1 umadutsa pakatikati pa mzindau,ndipo msewu uwu ndi wawukulu m'dziko lonse la Malaŵi.

Mzindawu udayamba moyo wake ngati mudzi wawun'gono chabe mphepete mwa mstinge wawukulu wa Lilongwe,pomwe udatengedawa ndi atsamunda a ku Mangalande,omwe udakhazikitsidwa ngati likulu lawoBritish colonial administrative centre. Nthawi yomwe izi zidachitika koyambilila kwa zaka za 1900. Chifuka chakuti mzindawu umapezeka pa njira yochoka ku mpoto ndi kulowela ku m'mwela kwa dziko la malawi,ndiponso pa mseu wopita ku Northen Rhodesia (tsopano Zambia),mzinda wa Lilongwe udakhala mzinda wawukulu zedi ku Malawi. Mu chaka cha 1974, Kapitolo ya dziko la Malawi idasunthidwa ku choka ku Zomba kupita ku boma la lilongwe. Ngakhale mzinda wa Lilongwe ndi kapitolo ya dziko la Malawi,ntchito za mbiri za chuma ndi malonda zi machitika mu mzinda wawukulu mu dziko lonse la Malawi, Blantyre (the commercial capital of Malawi. Mu nthawi za posachedwa pompa, Paliyamenti idasamutsidwa kuchoka ku Zomba ndipo ndikukhazikitsidwa mu mzinda wa Lilongwe. Izi adapanga ndi mtogoleri yemwe akulamla dziko la Malawi panopo, Dr Bingu wa Mutharika, ndipo mamembala a paliyamentiyi amayenera kukhala ku Lilongwe,kwa nthawi yomwe paliyamenti ikukumana. Tsopano Lilongwe ndi pakati kati pa za ndale,pamene Blantyre ndi pakati kati pa za malonda.

Chiwerengero cha anthu (Demographics)

[Sinthani | sintha gwero]
Year Population[1]
Chaka 1977 98 718
Chaka 1987 223 318
Chaka 1998 800,000
Chaka 2008 1,499,000
Chaka 2009 1,600,000

Za Mzindawu

[Sinthani | sintha gwero]

Anthu ambiri ochoka ku mayikao a ku ulaya,South Africa ndi anthu akunja,ogwira ntchito kunja amakhala ku Lilongwe, ndiponso kuli ma NGOs ngati (Care International, Plan International, Concern Worldwide, , Population Services International, The UNC Project, World Camp, Baylor International AIDS Initiative, Baobab Health Partnership, WaterAID), ma gulu ena ochoka kunja ngati (Peace Corps, USAID, DFID,UNICEF, UNHCR, UNFAO, WFP), ndipo makampani ochoka kunja, makamaka opanga nchito zokhudzana ndi za fodya, amapezekanso Lilongwe. Ndipo pa chifukwa chimenechi,alendo ambiri ochoka ku mayiko akunja adzapeza kuti mzinda wa Lilongwe ndi wamsangala,ndipo wokondweresta kukhalamo. Mzinda wa Liongwe uli ndi ma shopu ambili a coffee,modyeramo,mabala,malo achisangalalo, ndi casino amapezekanso mu mzinda wa Lilongwe. lilongwe ndi Mzinda omwe uli ndi zipangizo zosiyanasiyana, pakuti munthu utha kupanga chilichonse chomwe ungapange mu mizinda ya kunja ngati Johhanesburg,Pretoria,Newyork, kapenanso London. Moyo ku Lilongwe ndi wapamwamba ndipo wopambana.

Koma chinthu chosakhala bwino ndi chakuti,anthu ambiri omwe amakhala ku Lilongweku ama khala moyo wovutika chifukwa chosowa ndalama,ndi nchito. Chiwerengero cha anthu ku Lilongwe chakula zedi pa chifukwa chakuti anthu ambiri aku mudzi (kuwonjezera ana a masiye) amapita ku Lilongwe pakufuna moyo wamtauni. Anthuwa amafunanso ntchito (zomwe nthawi zambiri sizimapezeka,ndipo amapezeka kuti akungokhala), ndikuyamba mabizinesi awo ang'ono ang'ono. Ngakhale pali kusiyana kwakukulu chonchi pakati pa anthu okhala mu mznda wa Lilongwe,anthuwa amakhala mwamtendere.

Nthawi yamvula ndi kuchoka miyezi ya November ndi April, ndipo nthawi imeneyi ku Lilongwe kumakhala kotentha,kwamatope ndipo ko biriwira kopambana. Miyezi ya June mpaka August kumakhakla kukuzizira zedi (mpkana ma digili okwana 6 nthawizina). Nthawi ya September mpaka October ndiyotentha.

Lilongwe ndi malo omwe akhudzidwanso ndi matenda a HIV/AIDS ku Malawi. Mpakana anthu okwana 20% okhala mkatikati mwa mzindawu ali ndi HIV (kachilombo koyambitsa matenda a AIDS).Chomvesta chisoni ndi chakuti NAC inapereka lipoti la kuti anthu omwe akufa kwambiri ndi matendawa ndi anthu ofunika ngati aphunzitsi,anthu omwe amgwra ntchito ku unduna wa za ulimi,asilikali ndi apolisi [1].Chinthu Chinanso chomwe chikuwononga mzinda waLilongwe ndi kudulidwa kwa mitengo ya chilengedwe. Pali chiopsenzo chakuti pofika chaka cha 2015 anthu a m'midzi yozungulira Lilongwe adzakhala opandilatu mitengo ya nkhuni. Mavuto awa akukhudzana kwambili ndi kukukala kopitirira muyeso kwa chiwerengero cha anthu mu mzindawu.

Pa Zambiri za nyengo ya ku Malawi,chitani click apa www.bbc.com/weather [2].

Reference

[Sinthani | sintha gwero]
  1. "World Gazetteer: Malawi: largest cities and towns and statistics of their population". Archived from the original on 2013-05-25. Retrieved 2013-05-25. Unknown parameter |dead-url= ignored (help)

Lilongwe