Chakufwa Chihana

From Wikipedia
Jump to navigation Jump to search

Chakufwa Chihana (23 April 1939 - 12 June 2006) anali wotakataka pa nkhani za ufulu wa anthu wongwira ntchito komanso wa ndale ku Malawi. Chihana anabadwira ku Kawiluwilu kumpoto kwa dzikoli pa ndipo anamwalira ku Johannesburg, South Africa.

Chihana anali wotsutsa boma pa nthawi ya ulamuliro wa President Hastings Kamuzu Banda ndipo anakhala kunja kwa dzikoli mokakamizidwa mu zaka za mma 1970 ndi mma 1980. Pa nthawiyi, Chihana anamangidwapo. CHihana analandira mphoto ya Robert F Kennedy ya anthu oteteza ufulu wa chibadidwe mu 1992.

Chihana anathandiza kuti boma la a Banda livomere kupanga chisankho cha referendum, chokuti dzikoli likhale la zipani zambiri. Anthu a dzikoli anabvomera kuti boma likhale la zipani zambiri. Pa chisankho chotsatira chosankha President wa dzikoli, chipani cha a Banda cha Malawi Congress Party sichinapambane ndipo chipani cha a Bakili Muluzi cha United Democratic Front chinapambana. Chipani cha a Chihana cha Alliance for Democracy chinakhala chachitatu pa chisankhochi.


A Chihana anakhala wachiwiri kwa mtsogoleri mu boma la a Muluzi my 1994-1996 ndi 2003-2004.