Jump to content

David Banda

From Wikipedia

Davide Banda ndi mwana amene Madonna, woyimba wina otchuka wa ku Amerika anamutenga kuti akhale mwana wake. David Banda anabadwira ku Mchinji m’dziko la Malawi pa 24 Sepitembala 2005. A Madonna analembetsa ku boma la Malawi kuti akufuna atamutenga mwanayu pa 10 Okotobala 2006 kuti akufuna atamutenga mwanayo. Banja la a Madonna linamutchula mwanayo kuti David Banda Mwale Cicconne Ricthie, potenga dzina lomwe anabadwa nalo mwanayo komanso kuphatikiza la a Madonna wo ndi la amuna awo a Guy Ritchie. Mwanayo anakamupeza ku malo osungila ana amasiye pamene a Madonna anapita ku Malawi.

Davide Banda anatengedwa kuchoka ku Malawi pa 16 Okotobala. Kumutenga kwa mwanayu ndi a Madonna kunayambitsa nkhani yofufuza ngati a Madonna wo anapatsidwa ulemu wa padera chifukwa choti ndi munthu wotchuka. Izi zinali chomwechi chifukwa chakuti pa Malamulo a dzikoli, munthu amayenera kukhala mu dzikoli kwa chaka chimodzi asanatenge mwana. Ma gulu ena owona za ufulu wa anthu ananena kuti chaka cha 2005 ana atatu wokha analoledwa kutengendwa mdzikoli. Maguluwa anakasuma ku khothi kuti nkhaniyi iwunikidwenso bwino.

A Madonna anayankhula pa kanema pa pologilamu ya Oprah Winfrey pa 25 Okotobala 2006 pofuna kukana zomwe anthu ankanenazi. Pamene ankacheza ndi Oprah Winfrey, a Madonnawa ananena kuti ku Malawi kulibe malamulo olembedwa bwino bwino okhudza kutengedwa kwa ana osowa kapena amasiye ndi anthu ochokera kunja. Iwo anaonjeza kuti anakhala akuganiza zokatenga mwana kwa zaka ziwiri. A Madonna anatinso Banda anali akudwala chibayo komanso anali atachila malungo ndi chifuwa chachikulu ndiponso kuti iwowo anamupeza mwanayu ku malo osungirako ana a masiye. A Madonna anadandaulanso kuti atolankhani sathandiza ana amasiye a ku Malawi komanso a pa dziko lonse la pansi chifukwa amalemba nkhani zomwe sizilimbikitsa anthu kuti adzikatenga ana a masiye ku Africa. A Madonna anawonjeza kuti “Ndakhala ndikuganiza kwa nthawi yaitali kuti ndikatenge mwana wosowa ku dziko lina losauka- osati ku Malawi kokha- kuti ndimpatse moyo wabwino womwe iyeyo sakanatha kukhala nawo.”

David Bandayu sanali mwana wa masiye koma bambo ake anakamusiya ku malo osunga ana amasiye pamene mayi ake anamwalira. Pa 22 Okotobala 2006, ma nyuzipepala analemba kuti bambo ake a David, a Yohane Banda, samadziwa kuti mwana wawoyo akumupelekelatu kwa a Madonna ndipo sanazindikire kuti mawu oti adoption amatanthauza zimenezi. Iwo amayesa kuti mwanayo azikakhala kwa a Madonna kwa kanthawi kochepa kenaka nkubweleranso kwawo.

Patapita masiku ochepa a Madonna atawoneka pa pologilamu ya Oprah Winfrey, a Banda anadandaula kuti ma bungwe oona za ufulu wa anthu anakhala akuwabvutitsa tsiku ndi tsiku, ndi kumawopsyeza kuti sakudziwa chomwe akuchita. Iwonso anati “Cholinga cha mabungwewa akufuna kuti ineyo ndikaathandize pa mulandu umene iwo anakasuma ku khothi koma ine sindingabvomere zimenezi chifukwa ndikudziwa zomwe ndinagwirizana ndi a Madonna ndi amuna awo.”

A Madonna ananena pamene anafunsidwa ndi Meredith Vieira wa pa Dateline NBC kuti a Banda ankadziwa chomwe ankachita chifukwa iwo anakana kuti a Madona adzingowathandiza kulera mwanayo, koma iwowo anafuna kuti a Madonna amutenge mwanayo.

Panakali pano mulandu womwe anasuma mabungwe oona za ufulu wa anthu udakadikila chigamulo

External Links[Sinthani | sintha gwero]