Democratic Progressive Party

From Wikipedia
Jump to navigation Jump to search

Democratic Progressive Party (DPP) ndi chipani cha ndale cholamulira mu dziko la Malaŵi. Chipanichi chinakhazikitsidwa mu Febuluale 2005 ndi msogoleri wa dziko la Malaŵi, a Bingu wa Muntharika. Iwowa anayamba chipanichi chifukwa chakusagwirizana maganizo ndi chipani cha United Democratic Front (UDF) chomwe iwo anachiyimira pa chisankho. Panali maganizo ndi mphekesera zakuti boma la UDF lomwe linalamulira kuyambira 1994 mpaka 2004 silinachite zokwanira pothetsa mchitidwe wa ziphuphu.

Aphungu ena amene anapambana pa chisankho cha 2004 oyimira zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UDF analowa chipani cha DPP.

Chipani cha DPP chinapambananso pa chisankho cha Aphungu a Nyumba Ya Malamulo ndi Mtsogoleri wa dziko pa chisankho chomwe chinachitika pa 19 May 2009. Chipanichi chinapambana ndi mipando 140 mwa mipando 193 ya Nyumba ya Malamulo