Likodzo

From Wikipedia
Likodzo
Magulu ndiponso kumene kwachokera zinthu
ICD/CIM-10B65 B65
ICD/CIM-9120 120
DiseasesDB11875
MedlinePlus001321

Likodzo, lomwenso limadziwika ndi dzina lakuti matenda a munkhono, ndi matenda amene pachingelezi amatchedwanso helminthiasis ndipo amayambitsidwa ndi tizilombo kapena nyongolosi zophwathalala ngati tepi zomwe pachingelezi zimatchedwa schistosomes. Nyongolosi zimenezi nthawi zambiri zimakhala mu chikhodzodzo kapena mu matumbo. Zina mwa zizindikiro za matendawa ndi kumva kupweteka m'mimba, kutsegula m'mimba, chimbuzi cha magazi, kapena magazi mu mkodzo. Matenda a likodzo akafika poipa komanso munthu akakhala nawo kwa nthawi yaitali, zinthu zina m'thupi zikhoza kuwonongeka, monga chiwindi, impso, komanso akhoza kukhala wosabereka, kapena angayambe matenda a khansa ya m'chikhodzodzo. Ana omwe ali ndi matendawa amakhala ndi mavuto osiyanasiyana, monga kupinimbira ndiponso kulephera m'kalasi.[1]

Munthu angatenge matendawa ngati wakhudzana ndi madzi opanda mchere, a m'zithaphwi, mumtsinje kapena m'nyanja omwe ali ndi tizilimbo toyambitsa matendawa. Nkhono za m'madzi opanda mchere ndi zimene zimasunga tizilombo toyambitsa matenda a likodzo. Matendawa ndi ofala makamaka kwa ana a m'mayiko osauka chifukwa anawo amakonda kusewera m'madzi omwe angakhale ndi tizilombo toyambitsa matendawa. Anthu enanso amene amakhala pachiopsezo chachikulu chotenga matendawa ndi alimi, asodzi, ndiponso anthu onse amene amagwiritsa ntchito madzi osakhala aukhondo pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.[1] Matenda a likodzo ali m'gulu la matenda amene amayambitsidwa ndi nyongolosi kapena njoka za m'mimba.[2]Madokotala angadziwe ngati munthu ali ndi matendawa pomuyeza mkodzo kapena chimbudzi kuti aone ngati muli mazira a nyongolosi zoyambitsa matendawa. Njira inanso imene madokotala angatsatire ndi kuyeza magazi a munthuyo kuti aone ngati muli mazira a nyongolosi.[1]

Anthu angapewe matendawa ngati atamagwiritsa ntchito madzi aukhondo komanso ngati atayesetsa kuchepetsa chiwerengero cha nkhono. M'madera amene matendawa ndi ofala kwambiri, mankhwala a Praziquantel angamaperekedwe kwa anthu onse m'deralo kamodzi pa chaka. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti chiwerengero cha anthu amene angatenge matendawa chichepe komanso kuti matendawa asafalikire. Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse limalimbikitsanso anthu a m'madera amene matenda a likodzo ndi ofala kwambiri kuti azimwa mankhwala a Praziquantel.[1]

Pafupifupi anthu 210 miliyoni anali ndi matenda a likodzo padziko lonse m'chaka cha 2012.[3] Ndipo anthu oyambira pa 12,000[4] mpaka 200,000 amamwalira chaka chilichonse ndi matendawa.[5] Matendawa ndi ofala kwambiri ku Africa, ku Asia ndi ku South America.[1] Anthu pafupifupi 700 miliyoni a m'mayiko opitirira 70 amakhala m'madera amene matenda a likodzo ndi ofala kwambiri.[5][6] M'mayiko otentha, likodzo ndi matenda ofala kwambiri ndipo amangoposedwa ndi malungo okha pa matenda onse oyambitsidwa ndi tizilombo, ndipo amabwezera m'mbuyo kwambiri ntchito zachuma.[7] Matenda amenewa ali m'gulu la matenda amene amanyalanyazidwa kwambiri m'mayiko otentha.[8]

Malifalensi[Sinthani | sintha gwero]

  1. 1.0 1.1 1.2 1.3 1.4 "Schistosomiasis Fact sheet N°115". World Health Organization. 3 February 2014. Retrieved 15 March 2014.
  2. "Chapter 3 Infectious Diseases Related To Travel". cdc.gov. 1 August 2013. Retrieved 30 November 2014.
  3. Fenwick, A (Mar 2012). "The global burden of neglected tropical diseases". Public Health. 126 (3): 233–6. doi:10.1016/j.puhe.2011.11.015. PMID 22325616.
  4. Lozano, R.; Naghavi, M.; Foreman, K.; Lim, S.; Shibuya, K.; Aboyans, V.; Abraham, J.; Adair, T.; Aggarwal, R. (15 December 2012). "Global and regional mortality from 235 causes of death for 20 age groups in 1990 and 2010: a systematic analysis for the Global Burden of Disease Study 2010". Lancet. 380 (9859): 2095–128. doi:10.1016/S0140-6736(12)61728-0. PMID 23245604. Unknown parameter |displayauthors= ignored (help)
  5. 5.0 5.1 Thétiot-Laurent, S. A.; Boissier, J.; Robert, A.; Meunier, B. (27 June 2013). "Schistosomiasis Chemotherapy". Angewandte Chemie International Edition in English. 52 (31): 7936–56. doi:10.1002/anie.201208390. PMID 23813602.
  6. "Schistosomiasis A major public health problem". World Health Organization. Retrieved 15 March 2014.
  7. The Carter Center. "Schistosomiasis Control Program". Retrieved 17 July 2008.
  8. "Neglected Tropical Diseases". cdc.gov. 6 June 2011. Retrieved 28 November 2014.