Jump to content

Mangochi

From Wikipedia

Mangochi ndi mzinda omwe uli ku m'mwela kwa kwa dziko la Malawi. Mzindawu uli ku mapetopeto a ku m'wela a Lake Malawi. Mu nthawi ya atsamunda mzindawu unkadziwika ndi dzina lokuti Fort Johnstone. Kumathero kwa chaka cha 2008 mu mzinda wa Mangochi munali anthu pafupifupi 51,429.[1]

Mangochi ndi mzinda omwe udayambitsidwa ndi bwana m'kubwa a chitsamunda Sir Harry Johnston mu zaka za'ma 1890s ngati doko la chitetezo la atsamunda cha ku madzulo m'phepete mwa mstinge wa Shire[2] Kuchokera apa Fort Johnston – monga unkadziwikila mzindawu pa nthawiyi –udali mzinda omwe kunkayendetsedwa nkhani zokhudzana ndi kugulistidwa kwa anthu okagwira ntchito ya kalavula gaga m'mayiko a ku ulaya, komanso mzindawu unkagwira ntchito ngati koyendetserako boma la atsamunda.

  1. "2008,[world-gazetteer.com/home/malawi.php],Retrieved 2010-05-28.
  2. Mangochi, [Encyclopaedia Britannica], 2008, Retrieved 2011-05-28 .