Masauko Chipembere

From Wikipedia
Jump to navigation Jump to search

Henry Masauko Blasius Chipembere (5 August 1930 - 24 September 1974) anali mmodzi wa anthu amene anafuna kuti anthu a ku Malawi adzilamulire okha komanso anali mphunzitsi wa mbiri ku University ya UCLA.

Ntchito[edit | sintha gwero]

Ngati mmodzi wa anthu amene ankakhulupilira kuti anthu a ku Malawi adzilamulire paokha, a Chipembere anali mmodzi wa anthu a chipani cha Nyasaland African Congress, wachiwiri wa woyang'anira boma la Domasi. Dziko la Nyasaland litalandira ufulu wodzilamulira iwo anali msungichuma wa chipani cha Malawi Congress Party ndi nduna yoyang'anira za maboma aang'ono komanso nduna ya maphunziro.

Source[edit | sintha gwero]