Mtsinje wa Shire

From Wikipedia

Mtsinje wa Shire ndi mtsinje wa ku Malawi ndi Mozambique. Mtsinjewu umatuluka mu nyanja ya Malawi ndipo umalowa mu mtsinje wa Zambezi. Mtsinjewu ndi wautali ma kilomita 402 ndipo ukaphatikizidwa ndi nyanja ya Malawi ndi mtsinje wa Rukuru umakhala wa ma kilomita 1200. Kumtunda kwa mtsinjewu kumalumikizana ndi nyanja ya Malombe.

Zigwa za mtsinjewu ndi mbali ya zigwa za Great Rift Valley.