Phiri la Mulanje

From Wikipedia
Jump to navigation Jump to search
Phiri la Mulanje


Phiri la Mulanje ndi lodziwika kwambiri chifukwa cha maonekedwe ake wokongolo komanso njira zake zomwe ziri m’Phirimu zomwe ndi zochitsa kaso kwa iwo woyendamo. Ngakhale anthu ambiri wochokera kunja amabwera kudzakwera Phiri la Mulanje, koma ndi zomera ndi nyama zochepa zokha tikuzidziwa bwino za m’Phirimu. Apa tikuwona nyama zazing’onozing’ono zimene zimakhala m’tchire komanso m’mitengo ya m’nkhalango ya Phiri la Mulanje. Malo ambiri amene nyamazi zimapezeka chitetezo chawo chikuwopsezedwa ndipo tsogolo la nyamazi ndi lodetsa nkhawa.