Jump to content

Zathu

From Wikipedia

Zathu ikumangilira wayilesi, manyuzi, internet ndi zonse zokonda achisodzera M’malawi muno powapatsila show pawayilesi, nyimbo zomvera komanso nyimbo zapakanema.

Kuyambila pa 24 April sabata iliyonse Zathu Pawayilesi iziwulutsa maprogramu ake pa nyumba zinayi zowulutsa mawu: MBC Radio 2, Zodiak, Yoneco FM ndi Voice of Livingstonia.

Paphata penipeni pa ‘Zathu’ pali anthu 6 omwe akuyimila achinyamata muno Mmalawi monga: T-Reel- (Ovuta), Annetti (Wopulumuka m’mazunzo), Mphatso (Wolimba mtima), JP(Wosachedwa kukhuzidwa), Xander (Wamtima wabwino) ndi Chikondi (Wamaloto akuya).

Zathu pawayilesi ndi pulogalamu yomwe ili ndi sewero losanthula moyo wa achinyamata amene ayamba kupeza maubwezi ndi kutsatila maloto awo. Ilinso ndi nyimbo kuchokela ku band ya Zathu ndi maCelebu ena.

Palinso malangizo mu ‘Talk Show’ kuchokela kwa anthu achitsanzo (role models) muno M’malawi. Palinso “Gogo” yemwe akuyankha mafunso achinyamata komanso kupeleka malangizo..

Akukupatsilani pulogalamuyi ndi Lily B ndi DJ Goxy

Tsamba la painternet ya ‘Zathu’ www.zathu.mw mutha kulipeza pa facebook mwaulere, limenenso lizayambe kupezeka pa 17 April, 2017. Zathu ndiyathuyathu a Malawi ndipo ikupangidwa ndi a Malawi ndi thandizo lochokera ku Girl Effect.

Discography

[Sinthani | sintha gwero]

Nyimbo yomvera ndi kuonera, nkuphatikiza ndi sewero inatulutsidwa mu April, 2017.