Jump to content

Baibulo

From Wikipedia
Baibulo

Baibulo ndi buku lopatulika lomwe limakhulupiliwa kuti linapatsidwa kwa anthu kuchokera kwa Mulungu. Ilo lagawidwa muzigawo ziwiri- malemba a Chiheberi ndi malemba a Chigriki. Mabukhu amene amagwiritsidwa ntchito ku Chiyuda amatchedwa Tanaka kapena Baibulo la Chiyunda. Mabukhu amene amagwiritsidwa ntchito mu Chikhristu amatcheda Bukhu Loyera, Mau a Mulungu kapena Baibulo la chi Khristu. Chikhristu chimatenga ma bukhu ena a Baibulo la Chiyuda ku Chipangano cha kale, ngakhale ma bukhu awa amasiyana pa dongosolo lake ndipo ma baibulo ena ali ndi mabukhu owonjezera. baibulo la Chikhristu lili ndi mbali ina ya chiwiri yotchedwa Chipangano cha Tsopano.

Ma bukhu a baibulo amayalidwa mofanana mu zitanthauziro zosiyana siyana. Baibulo la Chikhristu linagawidwa mbali ziwili: Chipangano cha Kale ndi Chipangano cha Tsopano.

20